27/11/2025
Timudziwe Mussah Rashid; Kodi anakumana nazo zotani ku mpiraku? Werengani mwachidwi chonde.
Uyu ndi mussah Richard ochokela ku madeko, Iyeyu mpira wake anayambira kusewera mu Team ya Fish Eagle's ,amasewela kumbuyo wasewela kwa zaka zokwana zitatu.
Iyeyu amadziwika ndi dzina loti Boka, pochoka ku Fish Eagle's anazakhidwa athu 4 kupita ku Mangochi Medicals osewerawa ndi monga;
Mussah Rashid
Kasim Richard,
Ernest Thomas
Abudu Gaza
ku Mangochi Medicals wasewerako chaka chimodzi.
Kenako ulendo umapililiabe anasakhidwaso kuti akathandize kusewela team ya Cobe Barracks, kumeneko anapitako athu atatu;
Abudu Gaza
Kasimu Richard
Mussah Rashid
Team ya Cobe Barracks anaithandiza kwa zaka zitatu.
Koma chifukwa cha zovuta zina anachokako kubwelela kumudzi koma azake enawo anapitilizabe kusewelera Cobe.
Atabwelera kumudzi anabwelelaso ku Fish Eagle's koma uku sanachedweko anauamba ku sewera Beach ⛱️ soccer
Ndipo Team yakeyo inasakhidwa kuka menya nawo mpikisano wa Beach Soccer occer ku Salima mu chaka cha 2010 ndipo inafika nawo mundime yama semifinals ndipo ina gonjetsedwa ndi salima.
Iyeyu atabwerako ku Salima nkufika kwawo azibale ake anamuuza kuti kunadzafika muthu wina yemwe amafuna numbala yake, koma muthuyo anali ochokela ku Lilongwe pa n'thawi imeneyo sinazitengele mwachidule ananyalanyaza ndipo anabwelelaso ku timu ya Fish Eagle's.
Mu chaka cha 2011anazapita ku M'chinji kwa achibale ake, koma vuto kumeneko zampira sanka sangalatsidwa nazo anka funa tidzipanga za school komabe iye anakakamila mpila mpaka anapeza mwayi osewela team ya Mau Mau FC,
Ku Lilongwe sanakhalitse anabwelera kumudzi ndipo anapitilizabe kusewela Fish Eagle's.
Mu 2013 muthu waku Lilongwe uja anaimbaso fon ndikumuuza kuti pali team yomwe ikumufuna anyamuke atumiza transport,
Ndipo ananyamuka kupita ku Lilongwe koma team yomwe ankapitila sankaidziwa atafika analandilidwa bwino ndipo anandipatsidwa zipangizo zonse zoyenelela kwa osewera pa ground ndipo anadzidzimuka atamutengela ku timu ya Silver Strikers FC ndipo atafika anaona nzake wina amene ankamenya naye mpira ku Mau Mau Fc Aliki Zulu ndipo iye zinamupatsa chilimbikitso komaso chimwemwe.
Naye coach wa team yaikulu Stain Chirwa anamulandilanso mwa sangala ndipo mpila wake ku silver unayamba bwino kwambiri mpakana anandipasidwa contract ku team yaikulu ya zaka 4.
Mu chaka cha 2014 ndipamene anazyamba kumenyako ma game mwa apo ndi apo
First round itatha muchaka chomwecho anapatsidwa holiday nkupita kumudzi kukaona athu holiday itatha, anabwelelaso ku Silver mwa chimwemwe koma zomwe anakuma nazo sizimene ankayembekezela chifukwa kungofika ku training anauzidwa kuti team yawachotsa sanalipo ekha anali nda anzake monga
Aliki Zulu
Ndaona Dice
Samu Gunda komaso Yasin.
Ndipo n'thawi imeneyi ndiyomwe moyo anaumva kuwawa chifukwa analibe kulikose kochita, Maganizo ake anari osia mpila koma coach Stain Chirwa anamulimbitsa m'tima ndipo anamupezela mwai opita ku Karonga United Football Club panenepa anali osangalala kwambiri,
koma zomwe anakumana nazo sizomwenso ankayembekezela samalandila salary yake kuchokela ku Silver kwa miezi 8
Komaso ku Karonga sinkalandila ndalama iliose koma chifukwa mpila ankaukonda ankangopilila kuti mwina zisitha kutsogolo.
N'thawi yomwe anapita ku Karonga anali akwatila m'kazi nkumusiya ku Lilongwe chifukwa chosalandila ndalama m'kazi wake amazuzika kwambiri ataona kuti zithu siziku sitha anaganiza zobwelela ku Lilongwe maganizo osia mpila aja anabweraso kutengela ndi zomwe amadutsamo.
kenako muchaka cha 2016 anaitanidwa kuti akayese nawo mwai ku BLUE Eagles FC, Ma Eagle nthawi imeneyo coach anali
Dekereki Nsaka Kuona chilichose chinayenda bwino koma kuchoka kwa Nsakakuona ndikubwela makonyola chilichose Chinansitha apa ndipamene ndinangoganiza zosiya mpila chifukwa tsogolo silimaonekaso lokamenya Super League panopa sopano angomenya wamakwalala omweu umu ndim'mene mpila wake unayendela.
Pamene ena akudyelera nawo mpira Enatu anamva nawo 🤔 kuwawa chonde inu ZANU zikuyenda muziyamika Chauta.
Mwinatu nkutheka Inuso munadutsa munyengo yovutayi ku mbari ya mpirayi tipezeni ku inbox nanu nkhani yanu dziko liyidziwe.