10/06/2023
*π²πΌMu Chichewa*
*MPHAMVU YA KWACHA IGWETSEDWENSO - WATERO KAZEMBE WA πΊπΈUSA*
Katswiri pa nkhani za chuma a Betchani Tchereni ati zomwe zalankhulidwa ndi kazembe wa dziko la United states of America (USA) pankhani yogwetsa mphamvu ya Kwacha m'dziko muno sizachilendo.
Polankhulapo a Tchereni ati mphamvu ya Kwacha inachepa kale payokha ndipo kazembe wa dziko la USA angofuna kuti a Malawi avomereze.
A Tchereni ati Malawi ngati dziko limadalira katundu ogulitsa kunja ndipo pakadali pano mitengo ya katundu wambiri dziko muno idakwera.
Iwo ati kugwetsa mphanvu ya kwacha kungathe kuthandizira kubweretsa bata pa nkhani ya chuma m'dziko muno.
π MALAWI BREAKING NEWS24 π‘π²πΌπ²πΌ