11/11/2026
Ulendo opita ku Blantyre kuchoka ku Lilongwe wasokonekera atafika pa Phalura
Mai amene amayendetsa galimoto imeneyi anatenga matola pa tank ku Lilongwe malingana ndikuvuta kwa mafuta, magetsi, madzi, forex komaso kudura kwa katundu osiyana-siyana mdziko muno. Ndipo ali mkati mwa ulendo ananunkhiza kuopsa pakati pa anthu omwe anawanyamura poganizira kuti wina ananyamura mfuti kuti amupange chipongwe, maka pofuna kulanda galimoto.
Mayiyu ataganiza izi anazaganizaso mofulumira akuyendera chakwa Phalura ndipo anangoganiza zotsegura chitseko chake mkudumpha kuwasiya alendo aja kuti aziwonera okha.
Ndipo munthu amene anali kutsogolo atawona izi zachitika anaziwona ku tsogolo kukubwera truck yomwe ikadawombana ndi galimoto iyi, ndipo iye anayesetsa kugwira chiwongolero mkuipititsa ku tchire komwe inakawomba chibumi mkuima monga mukuyiwoneramu.
Pa ngozi iyi palibe wavulala modetsa nkhawa kuphakizapo mai amene amayendetsa ndipo anayitsikira pa njira atawona kuti sizimakatha bwino ngati akadapitiliza kukhara pa chiwongolero.