Afiki wa Labana ماشاالله

  • Home
  • Afiki wa Labana ماشاالله

Afiki wa Labana ماشاالله I'm anthlet of sports activities and l like to read Quran and Reasen Yes It's me

20/07/2023

I'm think to eat something else what do you think?.😂😂😂😂

04/01/2023
04/01/2023

Eti Nthawi Zina Munthu Umangoganiza Za Ndalama Zokha Basi

23/06/2022

Yes ma big

06/06/2022

*Superfecundation*
For the matured people(18 years and above)
Zimatheka mapasa (twins) kubadwa koma ali a bambo awiri osiyana. Ndipo izi zimachitika pa process(njira) yotchedwa Superfecundation. Liwu loti Superfecundatioń lidapangidwa kuchokera ku liwu la chi latin loti👉🏿 fecund lomwe limatanthauza kuti👉🏿 kupanga ana
Superfecundation is the fertilization of two or more ova from the same cycle by s***m from separate acts of sexual in*******se, which result to twin babies from two separate biological fathers. Superfecundation imachitika pamene mkazi waturutsa mazira awiri (ovulation) ndipo mazirawo akuyenda mu o***y mkaziyo mkugonana ndi mamuna ndipo mamunayo waombera umuna omwe walowa mu dzira limodzi, pasadathe 24hours mkaziyo mkugonananso ndi mamuna winanso ndipo mamuna wina uja mkuomberanso umuna mu dzira lina lotsala lija ndipo mazira ose awiriwa mkupanga ana.
(Mzungu Wakuda representing star walero)

Pali mitundu iwiri ya Superfecundation

1: *Homopaternal superfecundation* iyi ndi process imene mazira awiri a mkazi amalandira umuna kuchokera kwa mamuna mmodzi koma mu nthawi zosiyana, ndipo dzira lilironse mwa mazirawa limapanga mwana ndipo zotsatira zake mkazi amadzabereka mapasa otchedwa kuti👉🏿 *fraternal twins*
2: *heteropaternal superfecundation* iyi ndi njira yomwe mapasa amabadwa ali paubale theka kutanthauza kuti mapasawo amakhala half pachibale chifukwa amakhala ana a mayi mmodzi koma bambo awo ali osiyana ndipo iwo amabadwa munjira ndafotokoza pamwambapo.
Potengera za normal, panthawi yomwe umuna oyamba walowa mu dzira la mkazi, thupi limaimitsa ovulation kutanthauza kuti thupi limaimitsa dzira lotsala lija kuti lisayendenso kuopetsa kuti lingakumanenso ndi umuna wina koma nthawi zima zimapezeka kuti dzira lotsala lija laturukabe ndipo mkukumananso ndi umuna omwe umapanga mwana, kawirikawiri, ana obadwa pa process ya Superfecundation amakhala osiyana maonekedwe, chonde mundimvetsetse ine sindikutanthauza kuti mapasa onse omwe amaoneka osiyana maonekedwe ndekuti anabadwa pa process yi ayi, ndikuti sinthawi zonse mapasa akakhala osiyana maonekedwe ndekuti bambo awo ndiosiyana.
Kafukufuku ozama adapeza kuti Superfecundation imachitika kwambiri kwa a mphaka, makoswe komanso agalu achisanjira kapena kuti agalu oyendayenda aja ndipo akuti agalu oyendayenda aja zimatheka kubereka ana ambiri koma aliyense ochokera kwa galu wa mamuna wina.
Pofuna kudziwa ngati ana ali ofanana kapena osiyana bambo pali njira yoyeza yomwe imatchedwa *paternal testing*
Mukhale ndi tsiku labwino.
Mzungu Wakuda 0881403010

06/06/2022

Zimatheka mapasa (twins) kubadwa koma ali a bambo awiri osiyana. Ndipo izi zimachitika pa process(njira) yotchedwa Superfecundation.
Koma tisadafotokoze zimenezi tiyeni tikumbutsanenso kaye za 👉🏿 *Menstruation cycle*
*MENSTRUAL CYCLE AND OVULATION*.
( for the matured people, 13years & above )
Izi ndi za anthu okhawo omwe anakula, okhawo omwe ali ndi zaka 13 kapena kuposera apo.
*Star Walero family*
MENSTRUAL CYCLE AND OVULATION.
( for the matured people 13years & above )
Anthu ambiri samazimvetsetsa izizi kamba kakuti topic iyiyi inapatsidwa zizungu zozama kwambiri. Choncho kuphunzitsa izizi kumatheka ndithu koma anthu ambiri samazimvetsetsabe. Lero lino Mzungu Wakuda wangoganiza zophunzitsa topic iyiyi koma mu chilankhulo cha chichewa, akadzadziwa kulankhula Chitumbuka ndi Chiyao adzaiphunzitsanso mu zilankhulozi kuti aliyense yemwe adatha msinkhu azitsatirebe basi. Ndalemba topic yi kuti ithandize aliyense yemwe saitsata.
Anthu akazi tabwerani apa, amuna okwatira tamvetserani.
*. Munthu wamkazi aliyense yemwe ndi wamkulu amayenera azimvetsera thupi lake
*. Yambani kumalimvetsera thupi lanu ndikuona zinthu ziri mmusizi ndikutsimikizira kuti mwazionadi.
(Mzungu Wakuda +265881403010).
●MENSTRUAL PERIOD: iyi ndi nthawi yomwe magazi amaturuka ku maliseche a mkazi, nthawiyi ndi ija mumagwiritsa ntchito ma pad, ena thonje, ena mwiri, nthawi iyiyi ndiyo imatchedwa Menstrual Period.
●MENSTRUAL CYCLE:
Awa ndi masiku amene amatenga mkazi kuyembekezera kudzaonanso magazi ena, kapena kuti nthawi yomwe mkazi amakhala kuyembekezera kuturukanso magazi ena ku ndata kwake.
___Ngati munamaliza kupanga period yanu pa 10 August, ndipo idayambiranso pa 11 September. Ndekuti muli ndi *menstrual cycle* ya masiku 30(muwerenge kuyambira pa 10 August kulekeza pa 11 September)anthu ambiri tidauzidwa komanso kukhulupilira kuti mkazi ali ndi menstrual cycle ya masiku 28.
*Dziwani kuti* mkulakwitsa kwakukulu kukhulupilira zoti mkazi ali ndi menstrual cycle ya masiku 28, akazi ali ndi *Menstrual Cycle* zosiyanasiyana, menstrual za akazi zilipo zosiyanasiyana kuyambira masiku 21 mpaka kufikira masiku 35.
●OVULATION PERIOD:
Iyi ndi nyengo yomwe dzira limaturuka mu o***y, ndipo ovulation period ndi nyengo yomwe mkazi amatenga mimba mosakaikira. Nyengoyi ndi masabata awiri mutamaliza *menstrual period* kapena masiku a mkatikati mwa masabata awiri mukuyembekezera kuti mupange *menstrual period*.
√Mmusimu muli njira yophweka yomwe mungadziwire masiku amene mungatenge mimba ngati mutagonana ndi mamuna
(Unsafe period)
1. Kuchokera tsiku loyambilira limene mwayamba kuturuka magazi oonyeza period
2. Tengani Calendar ndi cholembera, kuyambira tsiku loyambiliraro, werengani masiku 15.
3. Chongani tsiku la nambala 15.
4. Chongani masiku atatu m'mbuyo mwa tsiku la nambala 15(kutanthauza tsiku la 12, 13 ndi 14). Chonganinso masiku atatu patsogolo pa tsiku la nambala 15 (kutanthauza kuti chongani masiku a 16,17 ndi la 18)
√.apa mupeza kuti muli ndi masiku 7 omwe mwachonga, loyamba kuchonga linali tsiku la nambala 15, kenaka la 12, 13, 14 ndi la 16, 17 komanso 18.
Masiku 7 omwe achongedwawa amenewa ndi masiku abwino kwa munthu yemwe mimba akuifuna koma ndioopsa kwa munthu yemwe sakufuna mimba, masikuwa ndi masiku amene ndi a nthaka, a chonde inde mimba imabwera mosavuta(fertile days, unsafe days). Masiku awawa ndiwo amatchedwa *ovulation days or fertile days*
ndipo kugonana ndi mamuna pa limodzi mwa masiku awawa pamakhala 98% umwayi otenga mimba.
✓•Mwezi ulionse muzipanga zimenezimasiku ena onse ndi masiku amene mimba siingabwere mwachisawawa
*Mwachitsanzo*
1. Munapanga period pa 10 August, kuyambira pa tsikuli tsiku la nambala 15 padzakhala pa 25 August tikawerenga kuyambira patsikuli. Ndekuti masabata awiri apita chichitireni period.
2. Masiku atatu pasanafike pa 25 August adzakhala masiku a pa 22, 23, ndi 24.
3. Masiku atatu kudusa pa 25 August adzakhala masiku a pa 26, 27 ndi 28.
4. Masiku 7 awa oyambira pa 22 August kurekeza pa 28 August ndimasiku omwe mazira amakhala kuti aturuka mu Ovary(ovulation days, fertile days), masikuwa kungogonana mosadziteteza mimba ibwera mosakaikiranso bola ngati bamboyo sadagwe mu mpapaya.
- masiku 7 wa mchikumbutso choti umuna umakhala masiku 7 mu thupi la mkazi, ndipo mukugonana zongafuna kusangalatsana mmasiku awawa china chake chotsamimwa chimabwera mosakaikiranso.
(Mzungu Wakuda)
Hey! Tamvetserani bwinobwino chifukwa Mzungu Wakuda akuyerabe.
@- ngati mukufuna mwana wa mkazi, gonanani masiku atatu aja mukuyembekezera *ovulation*(pa 22 kurekeza pa 24)
@- ngati mukufuna mwana wa mamuna gonanani mmasiku oyambira pa 25 kurekeza pa 28.
*Zizindikiro zosonyeza kuti Dzira laturka mu Ovary*(major signs of Ovulation)inuyo dekhani, sizikufunikira kuitana dokotala ayi, nokha mungathe kudziwa masiku amene amatchedwa ovulation days.
N**i zizindikiro zake.
1-kuphwanya kwa mutu
2- thupi limatentha kwambiri
3. Mawere amauma, makamaka nsonga za mawere, mawere amauma chimodzimodzi mukamaturuka magazi muja(period)
4. Chilakolako chofuna kugonana ndi mamuna chimakula.
5. Chiuno kuwawa
6. Mumamva fungo kwambiri, komanso mumaona kwambiri
7. Ku ndata kumaturuka ....
Nkhaniyi ndiyayitali ndthu... Ikupitilira. Tikumane kanthawi kena pamene ndimalize kufotokonza zimenezi.
Uthengawu ndiwabwinobwino. Chonde mungozitenga mkuzidziwa zinthu ndanenazi osati muloweze ndicholinga choti muzingopanga mchitidwe ogonana musali pa banja.
Dziwani kuti kugonana musali m'banja ndi kuchimwira Chauta ndipo adzakulangani. Inde ndikuti Allah sakondwera ndi mchitidwe ogonana musali pa banja ndipo mumamukwiyitsa mukamatero.
Kodi zimatheka bwanji mapasa kubadwa koma ali osiyana bambo. Superfecundation ndi.....
Next part loading,
Mzungu Wakuda akuti mukhale ndi mmawa wabwino

Chimwemwe Always Ife Kukwiya Sikutikhala Ai Inu Mukuona Bwanji Kkkkkk
28/01/2021

Chimwemwe Always Ife Kukwiya Sikutikhala Ai Inu Mukuona Bwanji Kkkkkk

28/01/2021

Nthawi Zina Kumachezako Ndi Anthu Allihamdullillah Poti Tili Moyo Kumanda Kulibe Kucheza Akudalitse Allah Azanga Onse.Koma Akutetezeni Kuzilango Zomwe Adatikozera

Address


Telephone

+27682126427

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Afiki wa Labana ماشاالله posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

  • Want your business to be the top-listed Photography Service?

Share